Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 8:9 - Buku Lopatulika

9 Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'mtsinje mokha?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chabwino, mungondiwuza nthaŵi yoti ndikupempherereni inu, nduna zanu ndi anthu anu omwe, kuti achuleŵa akuchokeni, achokenso m'nyumba mwanu, ndipo kuti akakhale mumtsinje mokha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mose anati kwa Farao, “Inu mungonditchulira nthawi imene mukufuna kuti ndikupempherereni, nduna zanu pamodzi ndi anthu anu kuti achule achoke mʼnyumba zanu ndi kuti atsale okhawo ali mu mtsinje wa Nailo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:9
8 Mawu Ofanana  

Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Baala, Dzisankhireni ng'ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza muchuluka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto.


Ndipo anafikira masiku asanu ndi awiri atapanda mtsinje Yehova.


Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu.


Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'mtsinje mokha.


Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.


Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.


Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako:


Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andichulukira kuti ndipereke Midiyani m'dzanja lao; angadzitame Israele pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa