Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
Eksodo 7:11 - Buku Lopatulika Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zitatero Farao adaitana anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo iwowo adachitanso zomwezo mwa matsenga ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. |
Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao.
Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.
Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoze; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.
ndipo m'mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yootcheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.
Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu.
Nayankha Daniele pamaso pa mfumu, nati, Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sangathe kuchiululira mfumu;
Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babiloni, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa lotoli.
pali munthu mu ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli;
Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.
chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama;
Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.
Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.
Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:
Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake.