Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 5:7 - Buku Lopatulika

7 Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu m'ufumuwu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mfumu inafuwula kuyitana owombeza, alawuli ndi amawula kuti abwere. Ndipo anawawuza anthu anzeru a ku Babuloni kuti, “Aliyense amene awerenge malembawa ndi kundiwuza tanthauzo lake adzavekedwa chovala cha pepo ndi mkanda wa golide udzavekedwa mʼkhosi mwake, ndipo adzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”

Onani mutuwo Koperani




Danieli 5:7
28 Mawu Ofanana  

Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.


Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye.


Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.


pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako, ndi mkanda pakhosi pako.


Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi, ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.


Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.


Lupanga lili pa Ababiloni, ati Yehova, pa okhala mu Babiloni, pa akulu ake, ndi pa anzeru ake.


Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m'manja mwako, ndi unyolo m'khosi mwako.


Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse mu ufumu wake wonse.


anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.


Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu.


Nayankha Daniele pamaso pa mfumu, nati, Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sangathe kuchiululira mfumu;


Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.


Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake.


Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama zakuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake.


pali munthu mu ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli;


Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake; koma sanakhoze kufotokozera kumasulira kwa chinthuchi.


Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.


Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anaveka Daniele chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wachitatu mu ufumumo.


popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.


Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.


Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.


Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa