3 ndipo m'mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yootcheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.
3 ndipo m'nyanjamo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yoocheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.
3 Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo.
Koma Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wake m'chipinda chogonamo. Momwemo Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wake wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.