Eksodo 6:11 - Buku Lopatulika Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pita kamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pita ukawuze Farao mfumu ya Igupto kuti awalole Aisraeli atuluke mʼdziko lake.” |
Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele.
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditse anthu anu konse.
Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako.