Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 6:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Pita ukawuze Farao mfumu ya Igupto kuti awalole Aisraeli atuluke mʼdziko lake.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Pita kamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 6:11
8 Mawu Ofanana  

Kotero tsopano, pita. Ine ndikukutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga, Aisraeli mʼdziko la Igupto.”


Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’


Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ”


Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”


Chipitireni changa kwa Farao kukamuyankhula mʼdzina lanu, iye wakhala akuzunza anthuwa, ndipo inu simunawapulumutse konse anthu anu.”


Kenaka Yehova anati kwa Mose,


anati, “Ine ndine Yehova. Umuwuze Farao mfumu ya Igupto zonse zimene Ine ndikuwuze iwe.”


Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona ine ndakuyika kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mʼbale wako Aaroni adzakhala mneneri wako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa