Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu; mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu.
Eksodo 5:12 - Buku Lopatulika Pamenepo anthuwo anabalalika m'dziko lonse la Ejipito kufuna chiputu ngati udzu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anthuwo anabalalika m'dziko lonse la Ejipito kufuna chiputu ngati udzu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero anthu aja adamwazikira m'dziko lonse la Ejipito kukafunafuna udzuwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero anthuwo anamwazikana mʼdziko lonse la Igupto kukamweta udzu. |
Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu; mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu.
Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzachepa pa ntchito yanu.
Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.
Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako.
Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.
Atumphako ngati mkokomo wa magaleta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.
Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati chiputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena.
Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.
Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu,