koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.
Eksodo 40:36 - Buku Lopatulika Ndipo pakukwera mtambo kuchokera ku chihema, ana a Israele amayenda maulendo ao onse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakukwera mtambo kuchokera ku Kachisi, ana a Israele amayenda maulendo ao onse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa maulendo ao onse, mtambo ukachoka pachihemapo, Aisraelewo ankachoka pamene analiripo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo. |
koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.
Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao.
Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;