Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:19 - Buku Lopatulika

19 koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiya m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokera usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Inu amene muli ndi chifundo chachikulu, simudaŵasiye m'chipululu iwowo. Mtambo umene unkaŵatsogolera poyenda m'njira masana sudaŵachokere, ndipo moto umene unkaŵaunikira njira poyenda usiku sudaŵasiye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 “Koma Inu ndi chifundo chanu chachikulu, simunawasiye mʼchipululu. Chipilala cha mtambo sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo masana ndipo chipilala cha moto sichinasiye kuwatsogolera pa njira yawo usiku.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:19
23 Mawu Ofanana  

Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.


Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva mu Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.


Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawathe, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo.


Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.


Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu; pakuti chifundo chake nchosatha.


Ndipo pakukwera mtambo kuchokera ku chihema, ana a Israele amayenda maulendo ao onse;


Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa chihema msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse.


Kumbukira zinthu izi, Yakobo; ndi Israele, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, sindidzakuiwala.


Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,


Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.


Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawathe onse m'chipululu.


Koma ndinabweza dzanja langa ndi kuchichita, chifukwa cha dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawatulutsa pamaso pao.


Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mzinda udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka.


Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;


Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.


ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa