Eksodo 40:32 - Buku Lopatulika pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi zonse akaloŵa m'chihema chamsonkhanomo, kapena kusendera ku guwalo, ankasamba, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose. |
Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi.
Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose.
Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.