Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri.
Eksodo 40:21 - Buku Lopatulika nalowa nalo likasa mu chihema, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nalowa nalo likasa m'Kachisi, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adaika bokosilo m'malo opatulika, ndipo adaika nsalu zochingira. Motero adachinga bokosi laumboni, monga momwe Chauta adamlamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye. |
Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri.
ndipo wansembeyo aviike chala chake m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika.