Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 4:16 - Buku Lopatulika

Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iye azikalankhula kwa anthu m'malo mwako. Adzakhala wokulankhulira, ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu ndiwe kwa Aroni.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye akayankhula kwa anthu mʼmalo mwako. Iye adzakhala wokuyankhulira ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu kwa iye.

Onani mutuwo



Eksodo 4:16
7 Mawu Ofanana  

Ndinati Ine, Inu ndinu milungu, ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.


Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;


Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.


ndipo Aroni anawafotokozera mau onse amene Yehova adauza Mose, nachita zizindikiro zija pamaso pa anthu.


Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.