Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.
Eksodo 39:42 - Buku Lopatulika Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israele anachita ntchito zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israele anachita ntchito zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Aisraele adachitadi ntchito zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose. |
Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.
Ndipo sanapatuke pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kalikonse, kapena za chumachi.
Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.
Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.
zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.
Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.
Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.