Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 39:41 - Buku Lopatulika

zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adabweranso ndi zovala zokongola kwambiri zoyenera kuvala ansembe potumikira m'malo oyera, zovala zopatulika za wansembe Aroni, ndiponso zovala za ana ake aamuna, zoyenera kuzivala pogwira ntchito zaunsembe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.

Onani mutuwo



Eksodo 39:41
7 Mawu Ofanana  

Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma.


Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi.


Ndipo usokere ana a Aroni malaya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.


ndi zovala zotumikira nazo, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakuchita nazo ntchito ya nsembe;


Ndipo anaomba zovala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zovala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.


nsalu zotchingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za ku chihema chokomanako;


Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israele anachita ntchito zonse.