Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 39:41 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

41 zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Adabweranso ndi zovala zokongola kwambiri zoyenera kuvala ansembe potumikira m'malo oyera, zovala zopatulika za wansembe Aroni, ndiponso zovala za ana ake aamuna, zoyenera kuzivala pogwira ntchito zaunsembe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 39:41
7 Mawu Ofanana  

Umusokere mʼbale wako, Aaroni, zovala zopatulika kuti azioneka mwaulemerero ndi molemekezeka.


Tsono umangirire mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi.


Upangirenso ana a Aaroni mwinjiro, malamba ndi nduwira kuti azioneka mwaulemu ndi molemekezeka.


ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe,


Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose.


nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano;


Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa