Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba, zovala zake nza malukidwe agolide.
Eksodo 39:3 - Buku Lopatulika Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya m'misiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adasula golide mwaphanthiphanthi, namlenzalenza, kuti amlukire kumodzi ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso la bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ntchito yaumisiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso. |
Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba, zovala zake nza malukidwe agolide.
ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;
Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.
Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga chihema ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri.
Ndipo anaomba efodi wa golide, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.