Eksodo 37:1 - Buku Lopatulika Ndipo Bezalele anapanga likasa la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Bezalele anapanga likasa la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Bezalele adapanga bokosi lachipangano ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Kutalika kwake kunali masentimita 114, muufupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. |
Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri.
chihema chokomanako, likasa la mboni, ndi chotetezerapo chili pamwamba pake, ndi zipangizo zonse za chihemacho;
ndipo analikuta ndi golide woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wa golide pozungulira pake.
Potero ndinapanga likasa la mtengo wakasiya, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m'phirimo, magome awiri ali m'manja mwanga.
okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;