Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Eksodo 34:23 - Buku Lopatulika Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, katatu chaka chimodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, katatu chaka chimodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amuna onse azibwera pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wa Aisraele, katatu pa chaka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka. |
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka: pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.
Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'zikondwerero zoikika, iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumpoto kudzalambira, atulukire njira ya kuchipata cha kumwera; ndi iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumwera, atulukire njira ya kuchipata cha kumpoto; asabwerere njira ya chipata anadzeracho, koma atulukire m'tsogolo mwake.
Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;
Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.