Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 34:24 - Buku Lopatulika

24 Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufika, ndi kukuziriza malire a dziko lanu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kulanda dziko lanulo nthaŵi zitatuzo za pa chaka, pamene mudzadziwonetse pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Ine ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufikako ndi kukulitsa malire anu. Palibe ndi mmodzi yemwe adzafune kulanda dziko lanu ngati inu muzidzapita katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, chaka chilichonse.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:24
19 Mawu Ofanana  

Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.


Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.


Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.


Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambane ndi Yehosafati.


Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.


Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.


ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;


Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Njira za munthu zikakonda Yehova ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.


Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; pakuti amitundu amene ndiwapirikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;


chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m'mzinda muno.


Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.


Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;


Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;


Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa