Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.
Eksodo 30:30 - Buku Lopatulika Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake aamuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake amuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka udzamdzoze Aroni pamodzi ndi ana ake, ndi kuŵapatula kuti akhale ansembe onditumikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Udzoze Aaroni ndi ana ake aamuna ndi kuwapatula kuti akhale ansembe onditumikira. |
Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.
Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.
Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.
nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.
Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.
Awa ndi maina a ana aamuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe.