Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 8:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake amuna, ndi zovala za ana ake amuna omwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Tsono Mose adatengako mafuta odzozera aja ndi magazi amene anali pa guwa, nawaza Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zao. Umu ndimo m'mene Mose adapatulira Aroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Kenaka Mose anatenga mafuta wodzozera ansembe ndi magazi amene anali pa guwa nawaza pa Aaroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zawo. Motero Mose anapatula Aaroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zawo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 8:30
15 Mawu Ofanana  

Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma.


Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.


Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake aamuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.


Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ake, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene Iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova;


limene Yehova analamula ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.


Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.


Awa ndi maina a ana aamuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe.


Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.


monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa