Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova?
Eksodo 30:15 - Buku Lopatulika Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wolemera asadzapereke kopitirira, ndipo wosauka asadzapereke mochepera pa theka la sekeli, pamene muzikapereka kwa Chauta zopereka zimenezi, kuti muwombole moyo wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu olemera asapereke koposa theka la sekeli ndipo osauka asapereke kuchepera theka la sekeli pamene mukupereka nsembe kwa Yehova yowombolera miyoyo yanu. |
Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova?
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.
Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zake, apereke choperekacho kwa Yehova.
Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.
Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.
Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.
Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.
Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.
Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama anachitacho; ndipo palibe tsankho.