Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 30:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndalama zoombolerazo zochokera kwa Aisraele, mudzagwiritse ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Zidzakumbutsa Chauta za Aisraele, ndipo zidzakhala zoombolera moyo wanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ulandire ndalama zopepeserazo kuchokera kwa Aisraeli ndipo zigwiritsidwe ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Zoperekazi zidzakhala chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova, ndiponso zowombolera miyoyo yanu.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 30:16
9 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera mu Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni?


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.


Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti,


chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.


Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku chihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova.


Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa