Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 31:50 - Buku Lopatulika

50 Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

50 Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

50 Ndipo ife tabwera ndi zopereka kwa Chauta zimene munthu aliyense adapeza, monga golide, zibangiri, zikono, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda, kuti achitire mwambo wopepesera machimo athu pamaso pa Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

50 Ndipo tabweretsa zopereka kwa Yehova zimene munthu aliyense anapeza: ziwiya zagolide, zibangiri, zigwinjiri, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda kuti tichitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 31:50
10 Mawu Ofanana  

Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!


Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?


Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.


Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.


Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.


Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.


nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife.


Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa