Aefeso 6:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Inu ambuye, muziŵachitiranso chimodzimodzi akapolo anu, ndipo muleke zoŵaopseza. Paja mukudziŵa kuti iwoŵa ndi inuyo, nonse muli ndi Mbuye wanu Kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho. Onani mutuwo |
Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?