Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Eksodo 29:5 - Buku Lopatulika Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono utenge zovala zija ndi kumuveka Aroni mwinjiro ndi mkanjo wautali wovala pamwamba pa efodi, ndiponso chovala chapachifuwa. Ndipo umange lamba woluka mwaluso uja m'chiwuno mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja. |
Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.
Pamenepo anasendera pafupi, nawanyamula osawavula malaya ao a m'kati, kunka nao kunja kwa chigono, monga Mose adauza.