Eksodo 28:15 - Buku Lopatulika15 Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 “Tsono usoke chovala chapachifuwa, chopetedwa mwaluso, chomavala poweruza. Mapangidwe ake akhale ngati a efodi, ndiye kuti a nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 “Upange chovala chapachifuwa chogwiritsa ntchito poweruza mlandu ndipo uchipange mwaluso kwambiri. Uchipange ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. Onani mutuwo |