Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:14 - Buku Lopatulika

14 ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 ndiponso maunyolo aŵiri a golide wokoma, opotedwa ngati zingwe, amene udzaŵalumikize ku zoikamozo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 ndiponso maunyolo awiri a golide wabwino kwambiri, wopetedwa ngati zingwe ndipo uwalumikize ku zoyikamozo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:14
9 Mawu Ofanana  

Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.


Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.


Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.


Ndipo upange zoikamo za golide;


Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.


Ndipo anapangira pachapachifuwa maunyolo ngati zingwe, ntchito yopota ya golide woona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa