Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 “Umsokerenso Aroni mwinjiro wa bafuta wokoma, ndipo umpangire nduŵira ya bafuta wokoma, ndiponso lamba wopetedwa mokongola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 “Uluke mwinjiro wa nsalu yofewa yosalala ndiponso upange nduwira ya nsalu yofewa yosalala. Lamba wake akhale wolukidwa bwino ndi munthu waluso.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:39
10 Mawu Ofanana  

Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga, anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.


Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.


Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.


Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;


ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.


Ndipo ubwere nao ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya am'kati.


Ndipo anaomba malaya a bafuta, a ntchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ake aamuna,


Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi.


Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa