Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israele azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israele azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Likhaledi pamphumi pake pa Aroni, motero asenze iye yemwe cholakwa chilichonse cha pa zopereka zimene Aisraele amazipatulira Chauta. Kuti Chauta alandire zopereka za anthuzo, Aroni azivala duŵali pa nduŵira yake nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Lidzakhala pa mphumi ya Aaroni, motero iye adzasenza cholakwa chilichonse cha pa zopereka zilizonse zimene Aisraeli amazipatulira Yehova. Aaroni azivala chikwangwanichi pa mphumi pake nthawi zonse kuti Yehova alandire zopereka za anthu ake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:38
21 Mawu Ofanana  

Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira.


Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.


Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.


naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa paguwa langa la nsembe; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.


Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.


Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.


Mwalekeranji kudya nsembe yauchimo m'malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulika kwambiri, ndipo Iye anakupatsani iyo, kuchotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwachitira chowatetezera pamaso pa Yehova?


ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova.


Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.


ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule.


Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako aamuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe.


M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.


kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa