Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:37 - Buku Lopatulika

37 Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Ulimange ndi kamkuzi kobiriŵira pa nduŵira ya Aroni, ndipo likhale cha kutsogolo kwa nduŵirayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Ulimange ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira ya Aaroni, ndipo duwalo likhale kutsogolo kwa nduwirayo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:37
10 Mawu Ofanana  

Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi.


Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha.


Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.


Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israele azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova.


Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.


ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.


Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.


Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo.


Nena ndi ana a Israele, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zovala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa