Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:36 - Buku Lopatulika

36 Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 “Upangenso duŵa la golide wabwino kwambiri, ulembepo mozokota mau akuti, ‘Choperekedwa kwa Chauta.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 “Upange duwa lagolide wabwino kwambiri kukhala ngati chidindo ndipo uzokotepo mawu akuti, choperekedwa kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:36
22 Mawu Ofanana  

Ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulika kwambiri, iye ndi ana ake, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kosatha.


Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya.


ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.


Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.


Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lake pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe.


Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira.


Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulochepo maina a ana a Israele;


ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.


Ndipo anaomba malaya a bafuta, a ntchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ake aamuna,


Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golide woona, nalembapo lemba, ngati malochedwe a chosindikizira, KUPATULIKIRA YEHOVA.


Namangako mkuzi wamadzi, kuumanga nao pamwamba pa nduwira; monga Yehova adamuuza Mose.


Malonda ake ndi mphotho yake zidzakhala zopatulikira Yehova; sizidzasungidwa kapena kuikidwa; chifukwa malonda ake adzakhala kwa iwo, amene akhala pamaso pa Yehova, kuti adye mokwana, navale chaulemu.


Lamulo la Kachisi ndi ili: pamwamba paphiri malire ake onse pozungulira pake azikhala opatulika kwambiri. Taonani, limeneli ndi lamulo la Kachisi.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.


Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.


Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.


Tsiku lomwelo padzaoneka pa miliu ya akavalo Opatulikira Yehova; ndi mbiya za m'nyumba ya Yehova zidzanga mbale za kuguwa la nsembe.


Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa