Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome.
Eksodo 27:7 - Buku Lopatulika Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ponyamula guwalo, mphikozo azizipisa m'mphete za pa mbali ziŵiri za guwalo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene mukunyamula guwalo, muzilowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo. |
Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome.
Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi mkuwa.
Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.