Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 30:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Upange mphete ziŵiri zagolide zonyamulira guwalo, ndipo uzilumikize ku guwa m'munsi mwa mkombero pa mbali ziŵiri, kuti mphiko zipisidwe m'mphetezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Upange mphete ziwiri zagolide ndipo uzilumikize ku guwa mʼmunsi mwa mkombero, mphete ziwiri ku mbali zonse ziwiri zoyangʼanana. Mphetozo zizigwira nsichi zonyamulira guwalo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 30:4
8 Mawu Ofanana  

Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.


Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo.


Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome.


Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide.


Ndipo ulipangire sefa, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngodya zake zinai mphete zinai zamkuwa.


Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.


Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira.


Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa