Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.
Eksodo 27:6 - Buku Lopatulika Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi mkuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi mkuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange mphiko ya mtengo wa kasiya yonyamulira guwalo, ndipo uikute ndi mkuŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndipo uzikutire ndi mkuwa. |
Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Nuwaike pansi pa khoma lamkati la guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo.
Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.
Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.