Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri.
Eksodo 26:34 - Buku Lopatulika Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulika kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulika kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uike chivundikiro chija pa bokosi lachipangano ku malo opatulika kopambanawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri. |
Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri.
Ndipo uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m'likasamo.
Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;
Anayesanso m'kati mwa Kachisi m'tsogolomo, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m'mopatulika kwambiri.
ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.
ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.