Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 26:34 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

34 Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Uike chivundikiro chija pa bokosi lachipangano ku malo opatulika kopambanawo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:34
6 Mawu Ofanana  

Kumbuyo kwa Nyumbayo anadula chipinda chachitali mamita asanu ndi anayi. Chipindachi anachimanga ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka ku denga kuti chikhale chipinda chopatulika chamʼkati mwa Nyumba ya Mulungu ngati Malo Wopatulika Kwambiri.


Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse.


Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake.


Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”


Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.


Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa