Eksodo 24:5 - Buku Lopatulika Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adatuma Aisraele achinyamata kuti iwoŵa apereke nsembe zopsereza, ndi kupha ng'ombe kuti apereke nsembe zamtendere kwa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano. |
Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.