Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 24:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono adatuma Aisraele achinyamata kuti iwoŵa apereke nsembe zopsereza, ndi kupha ng'ombe kuti apereke nsembe zamtendere kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 24:5
7 Mawu Ofanana  

Mundisonkhanitsire okhulupirika anga, amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.


Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.


Ngakhale ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova ayenera kudziyeretsa kuopa kuti ndingadzawalange.”


Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa