Eksodo 22:2 - Buku Lopatulika Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo imenyedwa nʼkufa, amene wapha mbalayo sanalakwe. |
Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeze pakuboola, koma ponsepo.
M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo.
nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mzinda wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi;
Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.
Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;