Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 22:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo imenyedwa nʼkufa, amene wapha mbalayo sanalakwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:2
11 Mawu Ofanana  

Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.


Mbala zimathyola nyumba usiku, koma masana zimadzitsekera; izo zimathawa kuwala.


Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo, akuwakuwiza ngati kuti anali akuba.


Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo magazi a anthu osauka osalakwa. Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba. Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,


Pamene ndichiritsa Israeli, machimo a Efereimu amaonekera poyera ndiponso milandu ya Samariya sibisika. Iwo amachita zachinyengo, mbala zimathyola nyumba, achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.


Amakhamukira mu mzinda, amathamanga mʼmbali mwa khoma. Amakwera nyumba ndi kulowamo; amalowera pa zenera ngati mbala.


ndipo wobwezera choyipa nʼkumupeza kunja kwa mzindawo, wolipsirayo atha kumupha wolakwayo popanda kugamula mlandu wakupha.


Koma zindikirani ichi: Ngati mwini nyumba akanadziwa nthawi yanji ya usiku imene mbala imabwera, sakanagona ndipo sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe.


chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku.


Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa