Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.
Eksodo 21:12 - Buku Lopatulika Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, nayenso aphedwe ndithu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, iyenso ayenera kuphedwa. |
Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.
Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.
Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.