Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:52 - Buku Lopatulika

52 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Yesu anati kwa iye, “Bwezera lupanga lako mʼchimake, chifukwa onse amene amapha ndi lupanga adzafa ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:52
13 Mawu Ofanana  

Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu.


koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.


Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.


Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.


osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.


Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.


popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa