Eksodo 20:21 - Buku Lopatulika Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu ankaima kutali, Mose yekha ndiye adayandikira mtambo wamdima m'mene munali Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu. |
muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.
Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu.
Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,
Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.
(ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:
amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.