Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.
Eksodo 20:16 - Buku Lopatulika Usamnamizire mnzako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usamnamizire mnzako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Usachite umboni womnamizira mnzako.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Usapereke umboni womunamizira mnzako. |
Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.
Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.
Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama,
Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.
naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo;
Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.
achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;
osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,
Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.