Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 20:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Usapereke umboni womunamizira mnzako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Usamnamizire mnzako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Usamnamizire mnzako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 “Usachite umboni womnamizira mnzako.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 20:16
23 Mawu Ofanana  

ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,


“Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama.


Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.


Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi; koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.


Mboni yonama sidzalephera kulangidwa; ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.


Munthu wochitira mnzake umboni wonama, ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.


“ ‘Musabe. “ ‘Musamanamizane. “ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.


“ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu. “ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.


“ ‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.


Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?” Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama,


Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”


Iwo anabweretsa mboni zonama zimene zinati, “Munthu uyu akupitirirabe kuyankhula mawu onyoza malo oyera ndi malamulo.


Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse.


“Usapereke umboni womunamizira mnzako.


Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona.


Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino,


Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa