mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Eksodo 20:14 - Buku Lopatulika Usachite chigololo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usachite chigololo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Usachite chigololo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Usachite chigololo. |
mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.
Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.
Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.
Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wamwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,
Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama,
Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lililonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.