Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 2:11 - Buku Lopatulika

11 Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pakuti Mulungu amene adanena kuti, “Usachite chigololo”, adanenanso kuti, “Usaphe”. Ngati inu chigololo simuchita, koma kupha mumapha, ndiye kutitu mwachimwira Malamulo onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 2:11
11 Mawu Ofanana  

Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;


Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama,


Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.


Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako.


Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lililonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa