Malaki 2:15 - Buku Lopatulika15 Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Kodi suja Mulungu adakulenga, iwe ndi mkazi wako, kukhala mmodzi, thupi ndi mzimu womwe? Nanga pakutero Mulunguyo ankafuna chiyani? Ankafunatu ana ompembedza Iye. Motero samala moyo wako ndipo khala wokhulupirika kwa mkazi wako woyamba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako. Onani mutuwo |