Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Eksodo 20:11 - Buku Lopatulika chifukwa m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera. |
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga kumwamba ndi dziko lapansi m'masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu.
Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.
Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mzinda ine, ndidzakweza manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.
Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.
nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo;
Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.
Pakuti wanena pena za tsiku lachisanu ndi chiwiri, natero, Ndipo Mulungu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse.
nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi: